4. Ndipo ana a Israyeli anacita cotero, nawaturutsira kunja kwa cigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israyeli anacita.
5. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwamuna kapena mkazi akacita cimo liri lonse amacita anthu, kucita mosakhulupirika pa Yehova, nakaparamuladi;
7. azibvomereza cimo lace adalicita; nabwezere coparamulaco monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kucipereka kwa iye adamparamulayo.
8. Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere coparamulaco, coparamula acibwezera Yehovaco cikhale ca wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya cotetezerapo, imene amcitire nayo comtetezera.