Numeri 3:45-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.

46. Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli, akuposa Alevi, akaomboledwe,

47. ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);

48. nupereke ndarama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna.

49. Pamenepo Mose analandira ndarama zaom bola nazo kwa iwo akuposa aja adawaombola Alevi;

Numeri 3