26. Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yahaliyeli, ndiye kholo la banja la Ayahaliyeli.
27. Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.
28. Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efraimu.
29. Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Gileadi; ndiye kholo la banja la Agileadi,
30. Ana a Gileadi ndiwo: Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;