18. Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.
19. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.
20. Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.