Numeri 13:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo anadza ku cigwa ca Esikolo, nacekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.

24. Malowa anawacha cigwa ca Esikolo, cifukwa ca tsangolo ana a lsrayeli analicekako.

25. Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.

Numeri 13