11. Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amace, Taonani, Esau mkuru wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu, wosalala.
12. Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pace ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
13. Ndipo amace anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.
14. Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amace; amace ndipo anakonza cakudya cokolera conga cimene anacikonda atate wace.
15. Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;
16. ndipo anabveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ace ndi pakhosi pace posalala;
17. ndipo anapereka m'dzanja la mwana wace Yakobo cakudya cokoleraco, ndi mikate imene anaipanga.
18. Ndipo iye analowa kwa atate wace, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?
19. Ndipo Yakobo anati kwa atate wace, Ndine Esau mwana wanu wamkuru; ndacita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.