Danieli 3:28-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mthenga wace, napulumutsa atumiki ace omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu wao wao.

29. Cifukwa cace ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uli wonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, adzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.

30. Pamenepo mfumu inakuza Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, m'dera la ku Babulo.

Danieli 3