26. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, amene dzina lace ndiye Belitsazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwace?
27. Nayankha Danieli pamaso pa mfumu, nati, Cinsinsi inacitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuciululira mfumu;
28. koma kuli Mulungu Kumwamba wakubvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara cimene cidzacitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa:
29. Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za ico cidzacitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene abvumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani codzacitikaco.