Danieli 2:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

20. Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;

21. pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, acotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi cidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.

22. Iye abvumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.

23. Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ici tacifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.

24. Potero Danieli analowa kwa Arioki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babulo; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babulo, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.

25. Pamenepo Arioki analowa naye Danieli kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja.

26. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, amene dzina lace ndiye Belitsazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwace?

Danieli 2