3. Pakuti mkulu wa ansembe ali yense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka,
4. Ndipo iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;
5. amene atumikira cifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose acenjezedwa m'mene anafuna kupanga cihema: pakuti, Cenjera, ati, ucite zonse monga mwa citsanzoco caonetsedwa kwa iwe m'phiri.
6. Koma tsopano iye walandira citumikiro comveka coposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.
7. Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda cirema sakadafuna malo a laciwirilo.