9. Cimene makolo anu anandiyesa naco,Ndi kundibvomereza,Naona nchito zanga zaka makumi anai.
10. Momwemo ndinakwiya nao mbadwouwu,Ndipo ndinati, Nthawi zonse amasocera mumtima;Koma sanazindikira njira zangaiwowa;
11. Monga ndinalumbira m'ukali wanga:Ngati adzalowa mpumulo wanga!
12. Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
13. komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene paehedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi cenjerero la ucimo;
14. pakuti takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa ciyambi ca kutama kwathu kucigwira kufikira citsiriziro;
15. umo anenamo,Lero ngati mudzamva mau ace,Musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.