7. Kumbukilani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira citsiriziro ca mayendedwe ao mutsanze cikhulupiriro cao.
8. Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.
9. Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundu mitundu, ndi acilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi cisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo.
10. Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira cihema alibe ulamuliro wa kudyako.
11. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, cifukwa ca zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.