2 Timoteo 2:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ucite cangu kudzionetsera kwa Mulungu wobvomerezeka, wanchito wopanda cifukwa ca kucita manyazi, wolunjika nao bwino mau a coonadi.

16. Koma pewa nkhani zopanda pace; pakuti adzapitirira kutsata cisapembedzo,

17. ndipo mau ao adzanyeka cironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto;

18. ndiwo amene adasokera kunena za coonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwacitika kale, napasula cikhulupiriro ca ena.

19. Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi cukhala naco cizindikilo ici, Ambuye azindikira iwo amene ali ace; ndipo, Adzipatule kwa cosalungama yense wakuehula dzina la Ambuye.

20. Koma m'nyumba yaikuru simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.

2 Timoteo 2