1 Timoteo 3:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.

7. Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumcitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

8. Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a cisiriro conyansa;

9. okhala naco cinsinsi ca cikhulupiriro m'cikumbu mtima coona.

10. Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.

11. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.

12. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.

13. Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

1 Timoteo 3